CHOONADI
By Late Philip (Philrhema) Maida (May His Soul Rest in Peace)
Takulandirani ku banja la choonadi
Msonkhano wa kuunika
Ku msanamira ndi maziko a choonadi, Mzati ndi mchirikizo wa choonadi
Komwe sititanthauzira baibulo chifukwa cha ukachenjede wa maphunziro
Kapena chifukwa choti timatha kulemba ndi kuwerenga
Koma Mulungu anatsegula maso athu
Tione zinsisi zokundikidwa m’malemba
Kuwala kwa mau ake kunatifikira
Timvetsetse chuma cha zinsisi za Mulungu
Tidziwe choonadi, zenizeni za umulungu
Nkutheka nanunso mufuna mudziwe anga Pilato
Kuti kodi choonadi m’chiani?
Dikirani pomwepo ndikuyankhani
Mvetserani ndikuululirani
Ichi ndiye choonadi, ichichi ndiye choonadi
Chokhacho chomwe Mulungu akunena
Osati zomwe mukudziwa kapena zomwe munamva
Iai, koma zokhazo zomwe Atate akunena
Ndikudziwa Sarah waona zilumika
Ndikuvomereza ziwalo zake zachita tsemwe
Uchembere wamulaka
Komabe ichichi si choonadi
Chaka cha mawa, nyengo ngati yomweyi, Sarah adzaima
M’mawere ake akugwawa , mudzatumphuka mkaka wa chikwanekwane
Phoso la Isaki, chimenechi nthuni, ndiye choonadi
Chokhacho chomwe Mulungu akunena
Ndikuvomereza buthuli lasiya kuphethira
Ntchentche ya liwamba ikayandikiza ku diso lake
Mapapo ake asiya malonda a mpweya
Paja zikatere mumati watsamaya
Koma imeneyi ndi mfundo ya moyo chabe
Choonadi nachi
Msungwanayu sanafe, wangogona tulo
Mukuseka chifukwa simunafikepo pangapa
Muvomereza ndikaitana kuti ‘Talita Kumi’
Buthulo nkudzambatuka, pamenepo mudziwa
Kuti ndimanenachi n’choonadi.
Ichi ndiye choonadi
Siziri choncho pokhapokha Achikulirewo atatero
Ichi ndiye choonadi
Sitidera nkhawa ndi mfundo za moyo
Sitivutika ndi zooneka za mzeru zapadziko
Chifukwa choonadi, chinatipanga ife mfulu
Omasuka, kokuti sitingamangidwenso
Ichi ndiye choonadi
Ichichi, ndiye choonadi
Chomwe omwe achidziwa chimawapanga mfulu
Munadziwa chiyani mayi?
Choonadi kodi, kapena mfundo za moyo
Zakuti nthenda mukudwalayo simungachire ananena ndani?
Zakuti ndinu mphawi, kapunthabuye mwazitenga kuti?
Zokuti choipachi ndi cha ku mtundu
Nanunso muyenera kuchikumana ananena ndani?
Nanga zakuti simudzabereka munazimva kuti?
Munamva Choonadi kodi, kapena mfundo za moyo
Ananena ndi Mulungu kodi kapena wolengedwa
Lero lino ndikumemani mudziwe choonadi
Ndipo choonadi chidzakupangani inu mfulu
Wolenga dziko akuti chani za moyo wanu
Fufuzani mudziwe choonadi
Choonadi chimapepuza moyo mkatikati mwa mavuto
Okuona atagwira kunkhongo kuyembekezera choipa chikugwera
Choonadi chimakukhalitsa chete mafunde atakakala
Openyelera atayayasamula kukamwa yasaa!
Osamvetsa chikukulimbitsa mtima n’chiani
Ndi choonadi umapukusa njoka ku chala nkumaotha moto
Apambali maso atatong’ola tong’oo
Kuyembekezera utupa kapena ugwa mwadzidzidzi
Ndi choonadi nthuni, moyo umazuna
Okuona osamvetsa unabadwa bwanji?
Takulandirani alendo athu, Kuno ku Msonkhano wa Kuunika
Ku Msanamira ndi Maziko a choonadi, Mzati ndi mchirikizo wa choonadi
Mungokhala nafe sabata imodzi mudabwa
Kwenikweni mwezi musinthika
Mau a choonadi asanduliza moyo wanu ntheradi
Simudzakhalanso chimodzimodzi
3 comments
i remember this poem! one of the best that He performed at church! such talent. May His Soul Continue resting in peace
wow power ful
Amen